1Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino. Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
2Yamikani Mulungu wa milungu.
2Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
3Yamikani Ambuye wa ambuye,
3pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
4Iye yekhayo amene amachita zodabwitsa zazikulu,
4pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
5Amene mwachidziwitso chake anapanga mayiko akumwamba,
5pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
6Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi,
6pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
7Amene anapanga miyuni ikuluikulu,
7pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
8Dzuwa lilamulire usana,
8pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
9Mwezi ndi nyenyezi zilamulire usiku,
9pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
10Amene anakantha ana woyamba kubadwa a Igupto,
10pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
11Natulutsa Israeli pakati pawo,
11pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
12Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka,
12pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
13Amene anagawa Nyanja Yofiira pakati,
13pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
14Nadutsitsa Israeli pakati pa nyanjayo,
14pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
15Koma anakokolola Farao ndi ankhondo ake mʼNyanja Yofiira,
15pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
16Amene anatsogolera anthu ake mʼchipululu
16pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
17Amene anakantha mafumu akuluakulu,
17pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
18Napha mafumu amphamvu,
18pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
19Siloni mfumu ya Aamori,
19pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
20Ogi mfumu ya Basani,
20pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
21Napereka dziko lawo ngati cholowa,
21pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
22Cholowa cha mtumiki wake Israeli;
22pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
23Amene anatikumbukira ife anthu opeputsidwa,
23pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
24Amene anatimasula kwa adani athu,
24pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
25Amene amapereka chakudya kwa cholengedwa chilichonse,
25pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
26Yamikani Mulungu wakumwamba,
26pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.