1Salimo la Davide.Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse;ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
2Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyerandipo ndidzayamika dzina lanuchifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu,pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anukupambana zinthu zonse.
3Pamene ndinayitana, munandiyankha;munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.
3
4Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova,pamene amva mawu a pakamwa panu.
5Iwo ayimbe za njira za Yehova,pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.
7Ngakhale ndiyende pakati pa masautso,mumasunga moyo wanga;mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga,mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
8Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosathamusasiye ntchito ya manja anu.