1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Oterewa ndi oyipa ndipo ntchito zawo ndi zonyansa; palibe amene amachita zabwino.
2 Yehova kumwamba wayangʼana pansi, kuyangʼana anthu onse kuti aone ngati alipo wina wanzeru, amene amafunafuna Mulungu.
3 Onse atembenukira kumbali, onse pamodzi asanduka oyipa; palibe amene amachita zabwino, palibiretu ndi mmodzi yemwe.
3
4 Kodi anthu ochita zoyipawa sadziwa chilichonse? Akudya anthu anga ngati chakudya chawo ndipo satamanda Yehova?
5 Awo ali apowo, agwidwa ndi mantha aakulu, pakuti Mulungu ali mʼgulu la olungama.
6 Inu ochita zoyipa mumalepheretsa chikonzero cha anthu osauka, koma Yehova ndiye pothawirapo pawo.
6
7 Ndithu, chipulumutso cha Israeli chidzachokera ku Ziyoni! Pamene Yehova abwezeretsa ufulu wa anthu ake, Yakobo akondwere ndipo Israeli asangalale!
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.