Masalimo 142:1-7 NYCCL2016 - Bible AI

1Ndakatulo ya Davide, pamene iyeyo anali mʼphanga. Pemphero. Ndikulirira Yehova mofuwula; ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo.

2Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake; ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake.

2

3Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga, ndinu amene mudziwa njira yanga. Mʼnjira imene ndimayendamo anthu anditchera msampha mobisa.

4Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani; palibe amene akukhudzika nane. Ndilibe pothawira; palibe amene amasamala za moyo wanga.

4

5Ndilirira Inu Yehova; ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga, gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.”

6Mverani kulira kwanga pakuti ndathedwa nzeru; pulumutseni kwa amene akundithamangitsa pakuti ndi amphamvu kuposa ine.

7Tulutseni mʼndende yanga kuti nditamande dzina lanu.

7Ndipo anthu olungama adzandizungulira chifukwa cha zabwino zanu pa ine.

e>