Masalimo 149:1-9 NYCCL2016 - Bible AI

1Tamandani Yehova. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima.

2Israeli asangalale mwa mlengi wake; anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo.

3Atamande dzina lake povina ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe.

4Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake; Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa.

5Oyera mtima asangalale mu ulemu wake ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo.

5

6Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo, ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo,

7kubwezera chilango anthu a mitundu ina, ndi kulanga anthu a mitundu yonse,

8kumanga mafumu awo ndi zingwe, anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo,

9kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse.

9Tamandani Yehova.

e>