1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide mtumiki wa Yehova. Iye anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.Davide anati: Ine ndimakukondani Inu Yehova, mphamvu zanga.
2Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga;Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo.Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa.
3Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.
3
4Zingwe za imfa zinandizinga;mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
5Anandimanga ndi zingwe za ku manda;misampha ya imfa inalimbana nane.
6Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize.Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga;kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.
6
7Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi,ndipo maziko a mapiri anagwedezeka;ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
41Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa.Analirira kwa Yehova koma sanawayankhe.
42Ine ndinawaperesa ngati fumbi lowuluka ndi mphepo.Ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.
42
43Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa anthu;mwandisandutsa kukhala mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
44Alendo amadzipereka okha pamaso panga;akangomva za ine amandigonjera.