Masalimo 2:1-12 NYCCL2016 - Bible AI

1Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu? Akonzekeranji zopanda pake anthu?

2Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo; ndipo olamulira asonkhana pamodzi kulimbana ndi Ambuye ndi wodzozedwa wakeyo.

3Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo ndipo titaye zingwe zawo.”

3

4Wokhala mmwamba akuseka; Ambuye akuwanyoza iwowo.

5Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,

6“Ine ndakhazikitsa mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.”

7Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula: Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga; lero Ine ndakhala Atate ako.

8Tandipempha, ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako; malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.

9Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo; udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.”

9

10Kotero, inu mafumu, chenjerani; chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.

11Tumikirani Yehova mwa mantha ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.

12Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye; kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu, pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa. Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.

>