Masalimo 20:1-9 NYCCL2016 - Bible AI

1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.

2Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika; akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.

3Iye akumbukire nsembe zako zonse ndipo alandire nsembe zako zopsereza.

3Sela

4Akupatse chokhumba cha mtima wako ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.

5Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu, Yehova ayankhe zopempha zako zonse.

5

6Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake; Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.

7Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.

8Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa, koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.

8

9Inu Yehova, pulumutsani mfumu! Tiyankheni pamene tikuyitanani!

>