Masalimo 21:1-13 NYCCL2016 - Bible AI

1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu, chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka!

2Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake.

2Sela

3Inu munayilandira ndi madalitso ochuluka ndipo munayiveka chipewa chaufumu chagolide weniweni pa mutu wake.

4Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa masiku ochuluka kwamuyaya.

5Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu; Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.

6Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya, Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu.

7Pakuti mfumu imadalira Yehova; kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba, iyo sidzagwedezeka.

7

8Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse; dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu.

9Pa nthawi ya kuonekera kwanu mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha. Mu ukali wake Yehova adzawameza, ndipo moto wake udzawatha.

10Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi, zidzukulu zawo pakati pa anthu.

11Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawo sadzapambana;

12pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawo pamene mudzawaloza ndi mivi yanu.

12

13Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu, ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu.

e>