1Salimo la Davide. Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
2Amandigoneka pa msipu wobiriwira, amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
3amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake.
4Ngakhale ndiyende mʼchigwa cha mdima wakuda bii, sindidzaopa choyipa, pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditonthoza.