1Salimo la Davide. Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo, dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo;
2pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja ndi kulikhazika pamwamba pa madzi.
2
3Ndani angakwere phiri la Yehova? Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika?
4Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera, amene sapereka moyo wake kwa fano kapena kulumbira mwachinyengo.
5Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
6Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova; amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo.
6Sela
7Tukulani mitu yanu inu zipata; tsekukani, inu zitseko zakalekalenu, kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
8Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.
9Tukulani mitu yanu, inu zipata; tsekukani, inu zitseko zakalekalenu, kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
10Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Iye ndiye Mfumu yaulemerero.