1Salimo la Davide. Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga.
2Ndimadalira Inu Mulungu wanga. Musalole kuti ndichite manyazi kapena kuti adani anga andipambane.
3Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye sadzachititsidwa manyazi koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.
3
4Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova, phunzitseni mayendedwe anu;
5tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa, pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga, ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.
6Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu, pakuti ndi zakalekale.
7Musakumbukire machimo a ubwana wanga ndi makhalidwe anga owukira; molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine, pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.
7
8Yehova ndi wabwino ndi wolungama; choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.
9Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama ndipo amawaphunzitsa njira zake.
10Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.
11Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova, khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka.
12Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova? Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate.
13Iye adzakhala pa ulemerero masiku ake onse, ndipo zidzukulu zake zidzalandira dziko ngati cholowa chawo.
14Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa; amawulula pangano lake kwa iwowo.
15Maso anga ali pa Yehova nthawi zonse, pakuti ndi Iye yekha amene adzawonjola mapazi anga mu msampha.
15
16Tembenukirani kwa ine ndipo mundikomere mtima, pakuti ndili ndekhandekha ndipo ndikuzunzika.
17Masautso a mu mtima mwanga achulukirachulukira; masuleni ku zowawa zanga.
18Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga ndipo mufafanize machimo anga onse.
19Onani mmene adani anga achulukira ndi momwe chidani chawo ndi ine chakulira.
20Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa; musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndimathawira kwa Inu.
21Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze, chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu.
21
22Wombolani Israeli Inu Mulungu, ku mavuto ake onse!