Masalimo 27:1-14 NYCCL2016 - Bible AI

1Salimo la Davide. Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndi linga la moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?

2Pamene anthu oyipa abwera kudzalimbana nane kudzadya mnofu wanga, pamene adani anga ndi achiwembu andithira nkhondo, iwo adzapunthwa ndi kugwa.

3Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzaopa. Ngakhale nkhondo itayambika kulimbana nane, ngakhale nthawi imeneyo, ine ndidzalimbika mtima.

3

4Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova, ichi ndi chimene ndidzachifunafuna: kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova, ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.

5Pakuti pa tsiku la msautso Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo; adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.

6Kotero mutu wanga udzakwezedwa kuposa adani anga amene andizungulira; pa Nyumba yake ndidzapereka nsembe ndi mfuwu wachimwemwe; ndidzayimba nyimbo kwa Yehova.

6

7Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe.

8Mtima wanga ukuti kwa Inu, “Funafuna nkhope yake!” Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.

9Musandibisire nkhope yanu, musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo; mwakhala muli thandizo langa. Musandikane kapena kunditaya, Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.

10Ngakhale abambo ndi amayi anga anditaya Yehova adzandisamala.

11Phunzitseni njira yanu Inu Yehova, munditsogolere mʼnjira yowongoka chifukwa cha ondizunza.

12Musandipereke ku zokhumba za adani anga, pakuti mboni zambiri zauka kutsutsana nane ndipo zikundiopseza.

12

13Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi; ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.

14Dikirani pa Yehova; khalani anyonga ndipo limbani mtima nimudikire Yehova.

e>