2
3Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi; Mulungu waulemerero abangula, Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
4Liwu la Yehova ndi lamphamvu; liwu la Yehova ndi laulemerero.
5Liwu la Yehova limathyola mikungudza; Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
6Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe, Siriyoni ngati mwana wa njati:
7Liwu la Yehova limakantha ngati kungʼanima kwa mphenzi.
8Liwu la Yehova limagwedeza chipululu; Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
9Liwu la Yehova limapindapinda mibawa ndi kuyeretsa nkhalango. Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”