1Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu. Inu Yehova, achulukadi adani anga! Achulukadi amene andiwukira!
2Ambiri akunena za ine kuti, “Mulungu sadzamupulumutsa.”
2Sela
3Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza, Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
4Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera.
4Sela
5Ine ndimagona ndi kupeza tulo; ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.
6Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.
6
7Dzukani, Inu Yehova! Pulumutseni, Inu Mulungu wanga. Akantheni adani anga onse pa msagwada; gululani mano a anthu oyipa.
7
8Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso akhale pa anthu anu.