1Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu.Ndidzakukwezani Yehova,chifukwa mwanditulutsa kwakuya,ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.
2Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizondipo Inu munandichiritsa.
3Inu Yehova, munanditulutsa ku manda,munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.
3
4Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika;tamandani dzina lake loyera.
5Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawikoma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse;utha kuchezera kulira usiku wonse,koma chimwemwe chimabwera mmawa.