1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo;musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi;mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu.
6Koma ine ndimadana nawo amene amamamatira mafano achabechabe;ine ndimadalira Yehova.
7Ndidzakondwa ndi kusangalala mʼchikondi chanupopeza Inu munaona masautso angandipo mumadziwa kuwawa kwa moyo wanga.
8Inu simunandipereke kwa mdanikoma mwayika mapazi anga pa malo otakasuka.
8
9Mundichitire chifundo Inu Yehova pakuti ndili pa mavuto;maso anga akulefuka ndi chisoni,mʼmoyo mwanga ndi mʼthupi mwanga momwe mukupweteka.
10Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtimandi zaka zanga chifukwa cha kubuwula;mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso,ndipo mafupa anga akulefuka.
11Chifukwa cha adani anga onse,ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga;ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga.Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.
12Ine ndinayiwalika kwa iwo ngati kuti ndinamwalira;ndakhala ngati mʼphika wosweka.
13Pakuti ine ndamva zonena zoyipa za anthu ambiri;zoopsa zandizungulira mbali zonse;iwo akukonza chiwembu kuti alimbane nane,kuti atenge moyo wanga.