5Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu,sindinabise mphulupulu zanga.Ndinati, “Ine ndidzawululazolakwa zanga kwa Yehova,ndipo Inu munandikhululukiramlandu wa machimo anga.”
7Inu ndi malo anga obisala;muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizingandi nyimbo zachipulumutso.
7Sela
8Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo;ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.
9Usakhale ngati kavalo kapena bulu,zimene zilibe nzeru,koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu,ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.
10Zowawa ndi zambiri za anthu oyipakoma chikondi chosatha cha Yehovachimamuzinga munthu amene amadalira Iye.