1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kwa Yedutuni. Salimo la Davide.Ndinati, “Ndidzasamalira njira zangandipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe;ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekereronthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.”
4“Yehova ndionetseni mathero a moyo wangandi chiwerengero cha masiku anga;mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani.
5Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri,kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu;moyo wa munthu aliyense ndi waufupi.
5Sela
6Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku:Iye amangovutika koma popanda phindu;amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani.
6
7“Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani?Chiyembekezo changa chili mwa Inu.
8Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse;musandisandutse chonyozeka kwa opusa.