1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide.Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu,Inu Mulungu wa chilungamo changa.Pumulitseni ku zowawa zanga;chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.
2Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi?Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza?Sela.