1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi,kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.
2Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo.Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?
3Misozi yanga yakhala chakudya changausana ndi usiku,pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti,“Mulungu wako ali kuti?”
4Zinthu izi ndimazikumbukirapamene ndikukhuthula moyo wanga:momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu,kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungundi mfuwu yachimwemwe ndi mayamikopakati pa anthu a pa chikondwerero.
4
5Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga?Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?Yembekezera Mulungu,pakuti ndidzamulambirabe,Mpulumutsi wanga ndi
6Mulungu wanga.
6Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga kotero ndidzakumbukira Inukuchokera ku dziko la Yorodani,ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.
7Madzi akuya akuyitana madzi akuyamu mkokomo wa mathithi anu;mafunde anu onse obwera mwamphamvuandimiza.
7
8Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake,nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane;pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.
8
9Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa,“Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala?Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,woponderezedwa ndi mdani?”
10Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawopamene adani anga akundinyoza,tsiku lonse akunena kuti,“Mulungu wako ali kuti?”
10
11Bwanji ukumva chisoni,iwe mtima wanga?Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga?Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso,Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.