1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali.Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
2Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike,ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,
3ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu,ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.
3
4Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu,malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.
5Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa;Mulungu adzawuthandiza mmawa.