6Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.
6
7Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;imbirani Iye salimo la matamando.
8Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
9Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhanamonga anthu a Mulungu wa Abrahamu,pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;Iye wakwezedwa kwakukulu.