1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Ndakatulo ya Davide. Pamene anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ndipo anati, “Kodi Davide sakubisala pakati pathu.”Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu;onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu.
2Imvani pemphero langa, Inu Mulungumvetserani mawu a pakamwa panga.