Masalimo 55:1-23 NYCCL2016 - Bible AI

1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya Davide. Pa zoyimbira za zingwe. Mvetserani pemphero langa, Inu Mulungu, musakufulatire kupempha kwanga,

2mverani ndipo mundiyankhe. Maganizo anga akundisautsa ndipo ndathedwa nzeru

3chifukwa cha mawu a adani anga, chifukwa cha kupondereza kwa anthu oyipa; pakuti andidzetsera masautso ndipo akundizunza mu mkwiyo wawo.

3

4Mtima wanga ukupweteka mʼkati mwanga; mantha a imfa andigwera.

5Mantha ndi kunjenjemera zandizinga; mantha aakulu andithetsa nzeru.

6Ndinati, “Ndithu, ndikanakhala ndi mapiko ankhunda! Ndikanawulukira kutali ndi kukapuma.

7Ndikanathawira kutali ndi kukakhala mʼchipululu.

8Ndikanathamangira kumalo anga a chitetezo; kutali ndi mphepo yaukali ndi yamkuntho.”

8

9Sokonezani maganizo a oyipa, Inu Ambuye, tsutsani mawu awo; pakuti ine ndikuona chiwawa ndi mkangano mu mzinda.

10Usana ndi usiku iwo akuzungulirazungulira pa makoma ake; nkhwidzi ndi kuzunza kuli mʼkati mwake.

11Mphamvu zowononga zili pa ntchito mu mzinda; kuopseza ndi mabodza sizichoka mʼmisewu yake.

11

12Akanakhala mdani akundinyoza, ine ndikanapirira; akanakhala mdani akudzikweza yekha kutsutsana nane, ndikanakabisala.

13Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye, bwenzi langa la pondaapanʼpondepo, ndi amene ukuchita zimenezi.

14Mnzanga amene nthawi ina tinkasangalala pa chiyanjano chokoma ku nyumba ya Mulungu.

14

15Mulole imfa itenge adani anga mwadzidzidzi; alowe mʼmanda ali amoyo pakuti choyipa chili pakati pawo.

15

16Koma ine ndinafuwulira kwa Mulungu, ndipo Yehova anandipulumutsa.

17Madzulo, mmawa ndi masana ndimalira mowawidwa mtima, ndipo Iye amamva mawu anga.

18Iye amandiwombola ine osavulazidwa pa nkhondo imene yafika kulimbana nane, ngakhale kuti ndi ambiri amene akunditsutsa.

19Mulungu amene ali pa mpando wake kwamuyaya, adzandimenyera nkhondo; adzawatsitsa adani anga, chifukwa safuna kusintha njira zawo zoyipa ndipo saopa Mulungu.

19

20Mnzanga woyenda naye wathira nkhondo abwenzi ake; iye akuphwanya pangano ake.

21Mawu ake ndi osalala kuposa batala komabe nkhondo ili mu mtima mwake; mawu ake ndi osalala kwambiri kuposa mafuta, komatu mawuwo ndi malupanga osololoka.

21

22Tulani nkhawa zanu kwa Yehova ndipo Iye adzakulimbitsani; Iye sadzalola kuti wolungama agwe.

23Koma Inu Mulungu mudzawatsitsa anthu oyipa kulowa mʼdzenje lachiwonongeko; anthu okhetsa magazi ndi anthu achinyengo sadzakhala moyo theka la masiku awo,

23koma ine ndimadalira Inu.

e>