1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide, pamene anathawa Sauli kupita ku phanga.Mundichitire chifundo, Inu Mulungu mundichitire chifundo,pakuti mwa Inu moyo wanga umathawiramo.Ndidzathawira mu mthunzi wa mapiko anumpaka chiwonongeko chitapita.
2Ine ndikufuwulira kwa Mulungu Wammwambamwamba,kwa Mulungu amene amakwaniritsa cholinga chake pa ine.
3Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa,kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri.Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake.
3
4Ine ndili pakati pa mikango,ndagona pakati pa zirombo zolusa;anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi,malilime awo ndi malupanga akuthwa.