1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide.Kodi inu olamulira mumayankhuladi molungama?Kodi mumaweruza mwachilungamo pakati pa anthu?
2Ayi, mʼmitima mwanu mumakonzekera zosalungama,ndipo manja anu amatulutsa zachiwawa pa dziko lapansi.
3Ngakhale kuchokera tsiku lawo lobadwa oyipa amasochera;kuchokera mʼmimba ya amayi awo, iwo ndi otayika ndipo amayankhula mabodza.
4Ululu wawo uli ngati ululu wa njoka,ngati uja wa mphiri imene yatseka mʼmakutu mwake.
5Imene simva liwu la munthu wamatsenga,ngakhale akhale wa luso lotani munthu wamatsengayo.
5
6Gululani mano mʼkamwa mwawo, Inu Mulungu,Yehova khadzulani mano a mikango!