1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide.Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,kapena kundilanga mu ukali wanu.
2Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka;Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.
3Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu.Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?
3
4Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse;pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
5Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira;Amakutamandani ndani ali ku manda?
5
6Ine ndatopa ndi kubuwula;usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga;ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.
7Maso anga atupa chifukwa cha chisoni;akulephera kuona chifukwa cha adani anga.
7
8Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa,pakuti Yehova wamva kulira kwanga.