1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Mikitamu ya Davide yophunzitsira. Pamene anamenyana ndi Mesopotamiya ndi Aramu-Zoba, ndi pamene Yowabu anabwerera ndi kukantha Aedomu 12,000 mʼChigwa cha Mchere.Inu Mulungu mwatikanatu ife, ndipo mwatiwonongera otiteteza.Inu mwatikwiyira, tsopano tibwezeretseni mwakale!
2Inu mwagwedeza dziko ndipo mwalingʼamba,konzani mingʼalu yake pakuti ikugwedezeka kwambiri.
3Inu mwaonetsa anthu anu nthawi za mavuto;inu mwatipatsa vinyo amene watichititsa kudzandira.