1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Ndimvereni Mulungu pomwe ndikunena madandawulo anga; tetezani moyo wanga ku chiopsezo cha mdani.
2Ndibiseni ku chiwembu cha anthu oyipa, ku gulu laphokoso la anthu ochita zoyipa.
2
3Iwo amanola malilime awo ngati malupanga, amaponya mawu awo olasa ngati mivi.
4Iwo amaponya mivi yawo ali pa malo wobisala kwa munthu wosalakwa; amamulasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha.
4
5Iwo amalimbikitsana wina ndi mnzake pa chikonzero chawo choyipa, amayankhula zobisa misampha yawo; ndipo amati, “Adzayiona ndani?”
6Iwo amakonzekera zosalungama ndipo amati, “Takonza ndondomeko yabwino kwambiri!” Ndithu maganizo ndi mtima wa munthu ndi zachinyengo.
6
7Koma Mulungu adzawalasa ndi mivi; mwadzidzidzi adzakanthidwa.
8Iye adzatembenuza milomo yawoyo kuwatsutsa ndi kuwasandutsa bwinja; onse amene adzawaona adzagwedeza mitu yawo mowanyoza.
8
9Anthu onse adzachita mantha; adzalengeza ntchito za Mulungu ndi kulingalira mozama zomwe Iye wazichita.
10Lolani wolungama akondwere mwa Yehova ndi kubisala mwa Iye, owongoka mtima onse atamande Iye!