3Pamene tinathedwa nzeru ndi machimo,Inu munakhululukira mphulupulu zathu.
4Odala iwo amene inu muwasankhandi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu!Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu,za mʼNyumba yanu yoyera.
4
5Mumatiyankha ife ndi ntchito zodabwitsa zachilungamo,Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,chiyembekezo cha mathero onse a dziko lapansindi cha nyanja zomwe zili kutali kwambiri,
6amene munapanga mapiri ndi mphamvu zanu,mutadziveka nokha ndi mphamvu.
7Amene munakhalitsa bata nyanjakukokoma kwa mafunde ake,ndi phokoso la anthu a mitundu ina.
8Iwo amene akukhala kutali amaopa zizindikiro zozizwitsa zanu;kumene dzuwa limatulukira ndi kumene dzuwa limalowera.Inu mumafuna nyimbo zachimwemwe.
8
9Inu mumasamalira dziko lapansi ndi kulithirira;Inuyo mumalilemeretsa kwambiri.Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzikuti upereke tirigu kwa anthu,pakuti Inu munakhazikitsa zimenezi.
10Mwadzaza nthaka yake ndi madzi ndi kusalaza migula yake,mwayifewetsa ndi mvula yamawawa ndi kudalitsa mbewu zake.
11Inu mumaveka chaka ndi zinthu zochuluka,ndipo ngolo zanu zimasefukira ndi zinthu zochuluka.
12Malo a udzu a mʼchipululu amasefukira;mapiri avekedwa ndi chisangalalo.
13Madambo akutidwa ndi zowetandi zigwa zavekedwa ndi tirigu;izo pamodzi zikufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe.