Masalimo 67:1-7 NYCCL2016 - Bible AI

1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo. Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa, achititse kuti nkhope yake itiwalire.

2Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi, chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.

2

3Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.

4Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe, pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.

5Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.

5

6Nthaka yabereka zokolola zake; tidalitseni Mulungu wathu.

7Mulungu atidalitse kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.

>