1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane;adani ake athawe pamaso pake.
2Monga momwe mphepo imachotsera utsi; Inu muwawulutsire kutali.Monga phula limasungunukira pa moto,oyipa awonongeke pamaso pa Mulungu.
3Koma olungama asangalalendi kukondwera pamaso pa Mulungu;iwo akondwere ndi kusangalala.
3
4Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando,mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo;dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.
5Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
6Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja,amatsogolera amʼndende ndi kuyimba;koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.
29Chifukwa cha Nyumba yanu ku Yerusalemu,mafumu adzabweretsa kwa Inu mphatso.
30Dzudzulani chirombo pakati pa mabango,gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu.Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva.Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo.
31Nthumwi zidzachokera ku Igupto;Kusi adzadzipereka yekha kwa Mulungu.
31
32Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansiimbirani Ambuye matamando.
32Sela
33Kwa Iye amene amakwera pa mitambo yakalekale ya mmwambaamene amabangula ndi mawu amphamvu.
34Lengezani za mphamvu za Mulungu,amene ulemerero wake uli pa Israeliamene mphamvu zake zili mʼmitambo.
35Ndinu woopsa, Inu Mulungu mʼmalo anu opatulika;Mulungu wa Israeli amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu ake.