Masalimo 70:1-5 NYCCL2016 - Bible AI

1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pempho. Fulumirani Mulungu kundipulumutsa; Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.

2Iwo amene akufunafuna moyo wanga achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa; onse amene akukhumba chiwonongeko changa abwezedwe mopanda ulemu.

3Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,” abwerere chifukwa cha manyazi awo.

4Koma onse amene akufunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!”

4

5Koma ine ndine wosauka ndi wosowa; bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu. Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga; Inu Yehova musachedwe.

>