12Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira,wozunzika amene alibe wina womuthandiza.
13Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowandi kupulumutsa osowa ku imfa.
14Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawapakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake.
14
15Iye akhale ndi moyo wautali;golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye.Anthu amupempherere nthawi zonsendi kumudalitsa tsiku lonse.
16Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse;pamwamba pa mapiri pakhale tirigu.Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni;zichuluke ngati udzu wakuthengo
17Dzina lake likhazikike kwamuyaya,lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa.
17Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye ndipo iwo adzamutcha iye wodala.
18Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeliamene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.
19Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyayadziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake.Ameni ndi Ameni.
19
20Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese.