21Pamene mtima wanga unasautsidwandi kuwawidwa mu mzimu mwanga,
22ndinali wopusa ndi wosadziwa;ndinali chirombo chopanda nzeru pamaso panu.
22
23Komabe ineyo ndili ndi Inu nthawi zonse;mumandigwira dzanja langa lamanja.
24Inu mumanditsogolera ndi malangizo anundipo pambuyo pake mudzanditenga ku ulemerero.
25Kodi kumwamba ndili ndi yani kupatula Inu?Ndipo dziko lapansi lilibe chilichonse chimene ndimachilakalaka koposa Inuyo.
26Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka,koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wangandi cholandira changa kwamuyaya.
26
27Iwo amene ali kutali ndi Inu adzawonongeka;Inu mumawononga onse osakhulupirika pamaso panu.
28Koma kunena za Ine ndi kwabwino kukhala pafupi ndi Mulungu.Ndatsimikiza kuti Ambuye Yehova ndiwo pothawirapo pangandipo ndidzalalika ntchito zanu zonse.