1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo.Tikuthokoza Inu Mulungu,tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe,anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.
3Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera,ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba.
3Sela
4Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.
5Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba;musayankhule ndi khosi losololoka.’ ”
5
6Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulokapena ku chipululu.
7Koma ndi Mulungu amene amaweruza:Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.
8Mʼdzanja la Yehova muli chikhochodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera;Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansiamamwa ndi senga zake zonse.
8
9Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya;ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.
10Ndidzadula nyanga za onse oyipakoma nyanga za olungama zidzakwezedwa.