Masalimo 79:1-13 NYCCL2016 - Bible AI

1Salimo la Asafu. Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowerera mʼcholowa chanu; ayipitsa Nyumba yanu yoyera, asandutsa Yerusalemu kukhala bwinja.

2Iwo anapereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame zamlengalenga ngati chakudya, matupi a oyera mtima anu kwa zirombo za dziko lapansi.

3Akhetsa magazi monga madzi kuzungulira Yerusalemu yense, ndipo palibe wina woti ayike mʼmanda anthu akufa.

4Ife ndife chinthu chonyozeka kwa anansi athu, choseketsa ndi cholalatiridwa kwa iwo amene atizungulira.

4

5Mpaka liti Inu Yehova? Kodi mudzakwiya mpaka muyaya? Kodi mpaka liti nsanje yanu idzayaka ngati moto?

6Khuthulirani ukali wanu pa anthu a mitundu ina amene sakudziwani Inu, pa maufumu amene sayitana pa dzina lanu;

7pakuti iwo ameza Yakobo ndi kuwononga dziko lawo.

8Musatilange chifukwa cha machimo a makolo athu chifundo chanu chibwere msanga kukumana nafe, pakuti tili ndi chosowa chachikulu.

8

9Tithandizeni Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; tipulumutseni ndi kutikhululukira machimo athu chifukwa cha dzina lanu.

10Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuti, “Ali kuti Mulungu wawo?” Ife tikuona, zidziwike pakati pa anthu a mitundu ina kuti mumabwezera chilango chifukwa cha magazi amene anakhetsedwa a atumiki anu.

11Kubuwula kwa anthu a mʼndende kufike pamaso panu; ndi mphamvu ya dzanja lanu muwasunge amene aweruzidwa kuti aphedwe.

11

12Mubwezere kwa anansi athu kasanu nʼkawiri kunyoza kumene ananyoza Inu Ambuye.

13Pamenepo ife anthu anu, nkhosa za pabusa panu, tidzakutamandani kwamuyaya, kuchokera mʼbado ndi mʼbado tidzafotokoza za matamando anu.

e>