1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a gititi. Salimo la Asafu.Imbani mwachimwemwe kwa Mulungu mphamvu yathu;Fuwulani mokweza kwa Mulungu wa Yakobo!
2Yambani nyimbo, imbani tamboliniimbani pangwe wolira bwino ndi zeze.
2
3Imbani lipenga la nyanga ya nkhosa yayimuna pa mwezi watsopano,ndi pamene mwezi waoneka wonse, pa tsiku la phwando;
4ili ndi lamulo kwa Israeli,langizo la Mulungu wa Yakobo.
5Iye anapereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefepamene anatuluka kulimbana ndi Igupto,kumene tinamva chiyankhulo chimene sitinachidziwe.