Masalimo 82:1-8 NYCCL2016 - Bible AI

1Salimo la Asafu. Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu; Iye akuweruza pakati pa “milungu.”

2“Mudzateteza osalungama mpaka liti, ndi kukondera anthu oyipa?

3Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye; mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.

4Landitsani anthu ofowoka ndi osowa; apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.

4

5“Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse. Amayendayenda mu mdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.

5

6“Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu, nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’

7Koma mudzafa ngati anthu wamba; mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.”

7

8Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi, pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.

>