1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora.Malo anu okhalamo ndi okomadi,Inu Yehova Wamphamvuzonse!
2Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka,kufuna mabwalo a Yehova;Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwuliraMulungu wamoyo.
2
3Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo,ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa,kumene amagonekako ana akepafupi ndi guwa lanu la nsembe,Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
9Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu;yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu.
9
10Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzikuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000;Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wangakuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.
11Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango;Yehova amapereka chisomo ndi ulemu;Iye sawamana zinthu zabwinoiwo amene amayenda mwangwiro.
11
12Inu Yehova Wamphamvuzonse,wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.