Masalimo 86:1-17 NYCCL2016 - Bible AI

1Pemphero la Davide. Ndimvereni Yehova ndipo mundiyankhe, pakuti ndine wosauka ndi wosowa.

2Yangʼanirani moyo wanga, pakuti ndine wodzipereka kwa Inu. Inu ndinu Mulungu wanga; pulumutsani mtumiki wanu amene amadalira Inu. Inu ndinu Mulungu wanga.

3Mundichitire chifundo, Inu Ambuye, pakuti ndikuyitana Inu tsiku lonse.

4Bweretsani chimwemwe kwa mtumiki wanu, Ambuye, pakuti ndimadalira Inu.

4

5Inu Ambuye, ndinu wokhululuka ndi wabwino, wodzaza ndi chikondi kwa onse amene amayitana Inu.

6Yehova imvani pemphero langa; mvetserani kulira kwanga kofuna chifundo.

7Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu, pakuti Inu mudzandiyankha.

7

8Pakati pa milungu palibe wina wofanana nanu Ambuye; palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu.

9Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye; iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu.

10Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa; Inu nokha ndiye Mulungu.

10

11Ndiphunzitseni njira yanu Yehova, ndipo ndidzayenda mʼchoonadi chanu; patseni mtima wosagawikana kuti ndilemekeze dzina lanu.

12Ndidzakutamandani Ambuye Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse; ndidzalemekeza dzina lanu kwamuyaya.

13Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu kwa ine; mwandipulumutsa ku malo ozama a manda.

13

14Inu Mulungu wanga, anthu odzikuza akundithira nkhondo; anthu ankhanza akufuna kundipha, amene salabadira za Inu.

15Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.

16Tembenukirani kwa ine ndipo ndichitireni chifundo; perekani mphamvu zanu kwa mtumiki wanu ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.

17Mundionetse chizindikiro cha ubwino wanu kuti adani achione ndi kuchititsidwa manyazi, pakuti Yehova mwandithandiza ndi kunditonthoza.

e>