Masalimo 87:1-7 NYCCL2016 - Bible AI

1Salimo la Ana a Kora. Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;

2Yehova amakonda zipata za Ziyoni kupambana malo onse okhalamo a Yakobo.

3Za ulemerero wako zimakambidwa, Iwe mzinda wa Mulungu: Sela

4“Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni pakati pa iwo amene amandidziwa. Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi, ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”

4

5Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti, “Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye, ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”

6Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina: “Uyu anabadwira mʼZiyoni.” Sela

7Oyimba ndi ovina omwe adzati, “Akasupe anga onse ali mwa iwe.”

>