Masalimo 93:1-5 NYCCL2016 - Bible AI

1Yehova akulamulira, wavala ulemerero; Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu, dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.

2Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale; Inu ndinu wamuyaya.

2

3Nyanja zakweza Inu Yehova, nyanja zakweza mawu ake; nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo.

4Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri, ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja, Yehova mmwamba ndi wamphamvu.

4

5Malamulo anu Yehova ndi osasinthika; chiyero chimakongoletsa nyumba yanu mpaka muyaya.

>