1Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale; magombe akutali akondwere.
2Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira; chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.
3Moto umapita patsogolo pake ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse.
4Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse; dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.
5Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova, pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi.
6Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake, ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.
6
7Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi, iwo amene amanyadira mafano; mulambireni, inu milungu yonse!
7
8Ziyoni akumva ndipo akukondwera, midzi ya Yuda ikusangalala chifukwa cha maweruzo anu Yehova.
9Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi; ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.
9
10Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
11Kuwala kumafika pa anthu olungama, ndi chimwemwe kwa olungama mtima.
12Kondwerani mwa Yehova Inu olungama ndipo tamandani dzina lake loyera.