Masalimo 98:1-9 NYCCL2016 - Bible AI

1Salimo. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa; dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zamuchitira chipulumutso.

2Yehova waonetsa chipulumutso chake ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina.

3Iye wakumbukira chikondi chake ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli; malekezero onse a dziko lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

3

4Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi, muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera.

5Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze, ndi zeze ndi mawu a kuyimba,

6ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimuna fuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu.

6

7Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo, dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo.

8Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo, mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe;

9izo ziyimbe pamaso pa Yehova, pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo, ndi mitundu ya anthu mosakondera.

>