1Yehova akulamulira, mitundu ya anthu injenjemere; Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi, dziko lapansi ligwedezeke.
2Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova; Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
3Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri, Iye ndi woyera.
3
4Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera; mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.
5Kwezani Yehova Mulungu wathu ndipo mulambireni pa mapazi ake; Iye ndi woyera.
5
6Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake, Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake; iwo anayitana Yehova ndipo Iyeyo anawayankha.
7Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo; iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.
7
8Inu Yehova Mulungu wathu, munawayankha iwo; Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka, ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.
9Kwezani Yehova Mulungu wathu ndipo mumulambire pa phiri lake loyera, pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.