1Patapita masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo, ndi Yohane mʼbale wa Yakobo pa okha ndipo anakwera nawo pa phiri lalitali.
2Pamenepo Iye anasinthika maonekedwe ake pamaso pawo. Nkhope yake inawala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinayera kuti mbuu.
3Nthawi yomweyo Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo akuyankhulana ndi Yesu.
4Petro anati kwa Yesu, “Ambuye ndi bwino kuti ife tikhale pano. Ngati mufuna ndidzamanga misasa itatu umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.”
5Iye akuyankhulabe, mtambo owala unawaphimba, ndipo mawu ochokera mu mtambo anati, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimukonda ndipo ndikondwera naye kwambiri. Mumumvere Iye!”
6Ophunzira atamva zimenezi, anachita mantha nagwa pansi chafufumimba.
7Ndipo Yesu anabwera nawakhudza nati,
8Atayangʼana, sanaone wina aliyense kupatula Yesu yekha.
9Akutsika ku phiriko, Yesu anawalamula kuti,
10Ophunzira anamufunsa Iye kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kukhala woyamba kubwera?”
11Yesu anayankha kuti,
12
13Pamenepo ophunzira anazindikira kuti amawawuza za Yohane Mʼbatizi.
14Atafika ku gulu la anthu, munthu wina anamuyandikira Yesu ndi kugwada pamaso pake.
15Iye anati, “Ambuye, muchitireni chifundo mwana wanga akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Kawirikawiri iye amagwa pa moto kapena mʼmadzi.
16Ine ndinabwera naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa.”
17Yesu anayankha nati, “
18Yesu anadzudzula chiwandacho ndipo chinatuluka mwa mnyamatayo ndipo anachira nthawi yomweyo.
19Pamenepo ophunzira anabwera kwa Yesu mwamseri ndi kumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwandacho?”
20Iye anayankha kuti,
21Chiwanda cha mtundu uwu sichingachoke chabe koma ndi pemphero ndi kusala kudya.”
22Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Iye anawawuza kuti,
23
24Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, “Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?”
25Iye anayankha kuti, “Inde amapereka.”
26Petro anayankha kuti, “Kuchokera kwa ena.”
27