10Ophunzira ake anati kwa Iye, “Ngati umu ndi mmene zilili pa mwamuna ndi mkazi, kuli bwino kusakwatira.”
11Yesu anayankha kuti, “Si aliyense amene angavomere chiphunzitso ichi, koma kwa okhawo amene achimvetsetsa.
12Pakuti ena ndi akuti sangakwatire chifukwa anabadwa motero, ena ali motero chifukwa chofulidwa ndi anthu ndipo ena anawukana ukwati chifukwa cha ufumu wakumwamba. Iye amene angalandire ichi alandire.”
13Pamenepo anabwera nawo ana kwa Yesu kuti awasanjike manja ndi kuwapempherera. Koma ophunzira ake anadzudzula amene anabweretsa anawo.
14Yesu anati, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa.”
15Atasanjika manja ake pa anawo, anachokapo.
16Taonani mnyamata wina anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, ndi chinthu chiti chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndipeze moyo wosatha?”
17Yesu anayankha kuti, “Ukundifunsiranji Ine za chinthu chimene ndi chabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino. Ngati ukufuna kulowa mʼmoyo wosatha mvera malamulo.”
26Yesu anawayangʼana iwo nati, “Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka.”
27Petro anamuyankha Iye kuti, “Ife tinasiya zonse ndi kukutsatirani Inu! Nanga tsono ife tidzalandira chiyani?”
28Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti pa nthawi yokonzanso zinthu zonse, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake waufumu mu ulemerero wake kumwamba, inu amene mwanditsata Ine mudzakhalanso pa mipando khumi ndi iwiri yaufumu, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli.
29Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena bambo kapena mayi kapena mkazi, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine adzalandira madalitso ochuluka ndi kulandiranso moyo wosatha.
30Koma ambiri amene ali oyambirira adzakhala omalizira, ndipo ambiri amene ndi omalizira adzakhala oyambirira.”