1Yesu atamaliza kuyankhula zonsezi, anati kwa ophunzira ake,
2
3Pamenepo akulu a ansembe ndi akuluakulu anasonkhana ku nyumba ya mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa,
4ndipo anapangana kuti amugwire Yesu mobisa ndi kumupha.
5Ndipo anati, “Osati nthawi yaphwando chifukwa pangabuke chipolowe pakati pa anthu.”
6Yesu ali ku Betaniya mʼnyumba Simoni Wakhate,
7mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo.
8Ophunzira ataona izi anayipidwa nafunsa kuti, “Chifukwa chiyani akuwononga chotere?
9Mafuta amenewa akanatha kugulitsidwa pa mtengo waukulu, ndipo ndalama zake zikanaperekedwa kwa osauka.”
10Yesu podziwa izi anawawuza kuti,
11
12
13
14Pamenepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo wotchedwa Yudasi Isikarioti anapita kwa akulu a ansembe
15nafunsa kuti, “Kodi mundipatsa chiyani ngati nditamupereka Iye kwa inu?” Pamenepo anamuwerengera ndalama zokwanira masiliva makumi atatu.
16Kuyambira pamenepo Yudasi anafunafuna nthawi yabwino yoti amupereke Yesu.
17Pa tsiku loyamba laphwando la buledi wopanda yisiti, ophunzira anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonze kuti malo odyera Paska?”
18Iye anayankha kuti,
19Pamenepo ophunzira ake anachita monga momwe Yesu anawawuzira ndipo anakonza Paska.
20Kutada, Yesu ndi ophunzira ake khumi ndi awiriwo anakhala pa tebulo nʼkumadya.
21Akudya, Iye anati,
22Iwo anamva chisoni kwambiri ndipo anayamba kuyankhulana naye mmodzimmodzi nati, “Kodi nʼkukhala ine Ambuye?”
23Yesu anayankha nati,
24
25Ndipo Yudasi amene anamupereka Iye anati, “Monga nʼkukhala ine Aphunzitsi?”
26Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti,
27Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo nati,
28
29
30Atayimba nyimbo, anatuluka kupita ku phiri la Olivi.
31Pamenepo Yesu anawawuza kuti,
32
33Petro anayankha nati, “Ngakhale onsewa atakuthawani, ine ndekha ayi.”
34Yesu anayankha nati,
35Koma Petro ananenetsa nati, “Ngakhale kutakhala kufa nanu pamodzi, sindidzakukanani.” Ndipo ophunzira onse ananena chimodzimodzi.
36Kenaka Yesu anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo anawawuza kuti,
37Anatenga Petro ndi ana awiri a Zebedayo, ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika mu mtima.
38Pamenepo anawawuza kuti,
39Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi chafufumimba napemphera kuti,
40Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nawapeza ali mtulo. Iye anafunsa Petro kuti,
41
42Anachokanso nakapemphera kachiwiri kuti,
43Atabweranso anawapeza ali mtulo chifukwa zikope zawo zinalemedwa ndi tulo.
44Choncho anawasiya napitanso kukapemphera kachitatu nanenanso chimodzimodzi.
45Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nati kwa iwo,
46
47Akuyankhula choncho, Yudasi mmodzi mwa khumi ndi awiriwo anafika. Pamodzi ndi iye panali gulu lalikulu la anthu ali ndi mikondo ndi zibonga otumidwa ndi akulu a ansembe ndi akuluakulu.
48Womuperekayo anawawuziratu chizindikiro anthuwo kuti, “Amene ndidzapsompsona ndi iyeyo; mugwireni.”
49Pamenepo Yudasi anapita kwa Yesu nati, “Moni, Aphunzitsi!” Ndipo anapsompsona Iye.
50Yesu anayankha kuti,
51Pa chifukwa ichi, mmodzi wa anzake a Yesu anagwira lupanga lake, nalisolola ndi kutema wantchito wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake.
52Yesu anati kwa iye,
53
54
55Pa nthawi yomweyo Yesu anati kwa gululo,
56
57Iwo amene anamugwira Yesu anamutengera kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anasonkhana.
58Koma Petro anamutsatira Iye patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Analowa nakhala pansi pamodzi ndi alonda kuti aone zotsatira.
59Akulu a ansembe ndi akulu olamulira Ayuda amafunafuna umboni wonama wofuna kuphera Yesu.
60Koma sanathe kupeza uliwonse, angakhale kuti mboni zambiri zabodza zinapezeka.
61Ndipo zinati, “Munthu uyu anati, ‘Ndikhoza kupasula Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso mʼmasiku atatu.’ ”
62Pamenepo mkulu wa ansembe anayimirira nati kwa Yesu, “Kodi suyankha? Kodi umboni umenewu ndi otani umene anthu awa akupereka kukutsutsa Iwe?”
63Koma Yesu anakhalabe chete.
64Yesu anayankha nati,
65Pamenepo mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zake nati, “Wanyoza Mulungu! Tifuniranji mboni zina? Taonani, tsopano mwamva mwano wake.
66Mukuganiza bwanji?”
67Kenaka anamulavulira kumaso namumenya ndi zibakera. Ena anamumenya makofi.
68Ndipo anati, “Tanenera kwa ife, Khristu. Wakumenya ndani?”
69Tsopano Petro anakhala ku bwalo la nyumbayo, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye nati, “Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.”
70Koma iye anakana pamaso pawo nati, “Sindikudziwa chimene ukunena.”
71Kenaka anachoka kupita ku khomo la mpanda, kumene mtsikana wina anamuonanso nawuza anthu nati, “Munthu uyu anali ndi Yesu wa ku Nazareti.”
72Iye anakananso molumbira kuti, “Sindimudziwa munthuyu!”
73Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pamenepo anapita kwa Petro nati, “Zoonadi, ndiwe mmodzi wa iwo, popeza mayankhulidwe ako akukuwulula.”
74Pamenepo anayamba kudzitemberera ndipo analumbira kwa iwo nati, “Sindimudziwa munthu ameneyo!”
75Ndipo Petro anakumbukira mawu amene Yesu anayankhula kuti,